Wednesday, March 7, 2012

TIKU WOPENI MFUMU?

Kumva tinamva koma timasiya dala kufunsa
M'munda mwathu Kwanitu ndi kholophethe
Koma taleka dala kufutsa
Pakuti pa Mudzi pano zinthu zalimba
Zathina pa Kwiko ya Katunduru
Utakafumbi nawonso wasanduka Khoswe
Zalimba nayenso avale zilimbe Nkhoswe
Pakuti Gogo uja walimba, walimba Mtima Ndikusauka phungu
atadya pwechepweche wa Zenzere
Kodi okoma atani Gama?
Kodi! okoma atani Gama? Alakhuranji?
Pamene wosungulumwa padzana uja, wosumidwa uja
Lero wakhuta ntoliro.
Miburi yonse wagondera
Ati kutsekereza khambakamba.
Ati kukhalitsa chete Pumbwa?
Anga wulutse zaku nzinda.
Kumva timamva koma timasiya dala kufunsa
Mtemba mundamo wadzaoneni Koma tasiya dala kufutsa
Poti wantchito zamanja ake uja
Wa onetsera Chithumwa chake Mame ata dekha
Amuweluza ndani?
Poti akutsidya nawo atanganidwa ndi kususukira kakhuta gona
Msodzi naye wagwa Mdiwa la mikwingwilima.
Mwa zioneratu Anasi ozitengera ku Mtima
Ufulu wa Mkuyu mkati muli Nyerere.
Yazionetsera Nkhandwe ku ana
Ya vuladi Bweya wa Nkhosa uja.
Zifuyo zathu aziteteza ndiyani? Khutukumve imva zayani.

No comments:

Post a Comment